Song of Solomon 8

1Ukanakhala kuti ndiwe mlongo wanga,
amene anayamwa mawere a amayi anga!
Ndikanakumana nawe pa njira,
ndikanakupsompsona,
ndipo palibe wina aliyense akanandinyoza.
2Ndikanakutenga
ndi kukulowetsa mʼnyumba ya amayi anga,
amayi amene anandiphunzitsa,
ndikanakupatsa vinyo wotsekemera kuti umwe,
zotsekemera za makangadza.
3Mutu wanga watsamira dzanja lake lamanzere
ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.
4Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani:
musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa
mpaka pamene chifunire ichocho.
Abwenzi

5Kodi ndani uyo akutuluka ku chipululuyo,
atatsamira wokondedwa wakeyo?
Mkazi

Ndinakudzutsa pa tsinde pa mtengo wa apulosi,
pamenepo ndi pamene amayi anachirira,
pamenepo ndi pamene wokubereka anamva ululu pokubala iweyo.
6Undiyike pamtima pako ngati chidindo,
ngati chidindo cha pa dzanja lako;
pakuti chikondi nʼchamphamvu ngati imfa,
nsanje ndiyaliwuma ngati manda.
Chikondi chimachita kuti lawilawi
ngati malawi a moto wamphamvu.
7Madzi ochuluka sangachizimitse chikondi,
mitsinje singachikokolole chikondicho.
Ngati wina apereka chuma chonse
cha mʼnyumba mwake chifukwa cha chikondi,
adzangonyozeka nazo kotheratu.
Abwenzi

8Ife tili naye mlongo wathu wamngʼono,
koma alibe mawere,
kodi tidzamuchitira chiyani mlongo wathuyu
pa tsiku limene adzamufunsire?
9Ngati iye ndi khoma,
tidzamumangira nsanja ya siliva.
Ngati iye ndi chitseko,
tidzamutchinga ndi matabwa a mkungudza.
Mkazi

10Ine ndili ngati khoma,
ndipo mawere anga ndi nsanja zake.
Tsono mʼmaso mwa bwenzi langa
ndine wobweretsa mtendere.
11Solomoni anali ndi munda wampesa ku Baala-Hamoni;
iyeyo anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi,
aliyense mwa iwo ankayenera kupereka
ndalama zasiliva 1,000 mʼmalo mwa zipatso zake.
12Koma munda wanga wampesa ndi wangawanga ndiponso wa ine ndekha.
Iwe Solomoni, khala nazo ndalama zasiliva 1,000
ndipo ndalama zasiliva 200 ndi za amene akusamalira mundawo.
Mwamuna

13Iwe amene umakhala mʼminda
uli pamodzi ndi anzako,
ndilole kuti ndimve liwu lako!
Mkazi

14Fulumira wokondedwa wanga,
ndipo ukhale ngati gwape
kapena mwana wa mbawala
wothamanga mʼmapiri mʼmene mumamera mbewu zokometsera chakudya.
Copyright information for NyaCCL